Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ezara 6:14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 Tsopano akulu+ a Ayuda anali kupita patsogolo pa ntchito yomanga+ nyumbayo atalimbikitsidwa ndi ulosi wa mneneri Hagai+ ndi Zekariya+ mdzukulu wa Ido.+ Iwo anamanga nyumbayo ndi kuimaliza potsatira lamulo la Mulungu wa Isiraeli,+ ndi lamulo la Koresi,+ Dariyo,+ ndi Aritasasita+ mfumu ya Perisiya.

  • Hagai 2:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 “‘Koma tsopano limba mtima iwe Zerubabele. Limba mtima+ iwe Yoswa mwana wa Yehozadaki mkulu wa ansembe,’ watero Yehova.

      “‘Limbani mtima anthu nonse a m’dzikoli ndipo gwirani ntchito,’+ watero Yehova.

      “‘Pakuti ine ndili ndi inu,’+ watero Yehova wa makamu.

  • Hagai 2:21
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 21 “Uza Zerubabele bwanamkubwa wa Yuda kuti,+ ‘Ine ndigwedeza kumwamba ndi dziko lapansi.+

  • Zekariya 4:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 Ngakhale pataikidwa chopinga chachikulu ngati phiri+ pamaso pa Zerubabele,+ chidzasalazidwa kukhala malo athyathyathya. Ndithu iye adzabweretsa mwala wotsiriza wa pakona.+ Akadzatero anthu adzafuula+ kuti: “Koma mwalawu ndiye ndi wokongola bwanji! Koma ndiye ndi wokongola!”’”+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena