13 Nkhosa zanga ndidzazitulutsa+ pakati pa anthu a mitundu ina. Ndidzazisonkhanitsa pamodzi kuchokera m’mayiko ena ndi kuzibweretsa m’dziko lawo.+ Ndidzazidyetsa m’mapiri a ku Isiraeli, m’mphepete mwa mitsinje komanso m’malo onse a m’dzikolo okhalako anthu.+