Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Deuteronomo 29:24
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 24 Mitundu yonse idzanena kuti, ‘N’chifukwa chiyani Yehova wachitira dzikoli zimenezi?+ N’chifukwa chiyani mkwiyo wake wayaka kwambiri chonchi?’

  • Deuteronomo 30:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Yehova Mulungu wanu adzabweza kwawo anthu a mtundu wanu amene anagwidwa ndi kupita kudziko lina,+ ndipo adzakumverani chifundo+ n’kukusonkhanitsaninso pamodzi kuchokera pakati pa anthu onse kumene Yehova Mulungu wanu anakubalalitsirani.+

  • Yeremiya 23:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 “Ine ndidzasonkhanitsa pamodzi nkhosa zanga zotsala kuchokera m’mayiko onse kumene ndinazibalalitsira+ ndipo ndidzazibwezeretsa kumalo awo kumene zimadyera.+ Nkhosazo zidzaberekana ndi kuchuluka.+

  • Yeremiya 29:14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 Ndidzakulolani kuti mundipeze,’+ watero Yehova. ‘Ndidzasonkhanitsa anthu a mtundu wanu amene anagwidwa ndi kutengedwa kupita kumayiko ena ndipo ndidzakusonkhanitsani kuchokera m’mitundu yonse ndi kumalo onse kumene ndakubalalitsirani,’+ watero Yehova. ‘Kenako ndidzakubwezeretsani kumalo amene ndinakuchotsani ndi kukupititsani ku ukapolo.’+

  • Ezekieli 37:21
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 21 “Uwauzenso kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Ine nditenga ana a Isiraeli kuchokera pakati pa mitundu ina ya anthu kumene anapita. Ndidzawasonkhanitsa pamodzi kuchokera m’mayiko owazungulira ndipo ndidzawabweretsa m’dziko lawo.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena