21 Kenako ndinalamula kuti tisale kudya tili kumtsinje wa Ahava kuja, kuti tidzichepetse+ pamaso pa Mulungu wathu ndi kumupempha kuti atisonyeze njira yoyenera+ kwa ife, ana athu,+ ndi katundu wathu yense.
31 Pomalizira pake tinachoka pamtsinje wa Ahava+ pa tsiku la 12 la mwezi woyamba+ kuti tipite ku Yerusalemu. Dzanja la Mulungu wathu linali nafe pa ulendowu moti anatipulumutsa+ m’manja mwa adani ndiponso kwa achifwamba a m’njira.