13 Usikuwo ndinatulukira pa Chipata cha Kuchigwa,+ kutsogolo kwa Kasupe wa Chinjoka Chachikulu ndi kulowera ku Chipata cha Kumilu ya Phulusa.+ Pa nthawiyi, ndinali kuonetsetsa+ mmene mpanda wa Yerusalemu unawonongekera ndiponso mmene moto unawonongera zipata zake.+