Numeri 14:9 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 9 Chongofunika n’chakuti musam’pandukire Yehova.+ Komanso anthu a m’dzikolo musawaope,+ chifukwa ali ngati chakudya kwa ife. Alibenso chitetezo,+ koma ifeyo Yehova ali nafe.+ Musawaope ayi.”+ Deuteronomo 20:3 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 3 kuti, ‘Mverani Aisiraeli inu. Lero mukuyandikira adani anu kuti mumenyane nawo. Mitima yanu isachite mantha.+ Musaope ndipo musathawe mwamantha kapena kunjenjemera chifukwa cha iwo,+ Yoswa 1:9 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 9 Monga ndakulamula kale,+ ukhale wolimba mtima ndipo uchite zinthu mwamphamvu. Usachite mantha kapena kuopa,+ pakuti Yehova Mulungu wako ali nawe kulikonse kumene upiteko.”+ Salimo 27:1 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 27 Yehova ndiye kuwala+ kwanga ndi chipulumutso changa.+Ndingaopenso ndani?+Yehova ndiye malo a chitetezo cha moyo wanga.+Ndingachitenso mantha ndi ndani?+ Aroma 8:31 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 31 Ndiye tinene kuti chiyani pa zinthu zimenezi? Ngati Mulungu ali kumbali yathu, ndani adzatsutsana nafe?+ Aheberi 13:5 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 5 Moyo wanu ukhale wosakonda ndalama,+ koma mukhale okhutira+ ndi zimene muli nazo pa nthawiyo.+ Pakuti Mulungu anati: “Sindidzakusiyani kapena kukutayani ngakhale pang’ono.”+
9 Chongofunika n’chakuti musam’pandukire Yehova.+ Komanso anthu a m’dzikolo musawaope,+ chifukwa ali ngati chakudya kwa ife. Alibenso chitetezo,+ koma ifeyo Yehova ali nafe.+ Musawaope ayi.”+
3 kuti, ‘Mverani Aisiraeli inu. Lero mukuyandikira adani anu kuti mumenyane nawo. Mitima yanu isachite mantha.+ Musaope ndipo musathawe mwamantha kapena kunjenjemera chifukwa cha iwo,+
9 Monga ndakulamula kale,+ ukhale wolimba mtima ndipo uchite zinthu mwamphamvu. Usachite mantha kapena kuopa,+ pakuti Yehova Mulungu wako ali nawe kulikonse kumene upiteko.”+
27 Yehova ndiye kuwala+ kwanga ndi chipulumutso changa.+Ndingaopenso ndani?+Yehova ndiye malo a chitetezo cha moyo wanga.+Ndingachitenso mantha ndi ndani?+
31 Ndiye tinene kuti chiyani pa zinthu zimenezi? Ngati Mulungu ali kumbali yathu, ndani adzatsutsana nafe?+
5 Moyo wanu ukhale wosakonda ndalama,+ koma mukhale okhutira+ ndi zimene muli nazo pa nthawiyo.+ Pakuti Mulungu anati: “Sindidzakusiyani kapena kukutayani ngakhale pang’ono.”+