17 Pakuti Yehova Mulungu wanu ndi Mulungu wa milungu+ ndi Mbuye wa ambuye.+ Iye ndi Mulungu wamkulu, wamphamvu ndi woopsa,+ amene sakondera+ munthu aliyense ndipo salandira chiphuphu.+
8 Tsoka ife! Adzatipulumutsa ndani m’manja mwa Mulungu wamkuluyu? Ameneyu ndi Mulungu amene anakantha Iguputo ndi masautso amtundu uliwonse m’chipululu.+