3Ndiyeno Eliyasibu+ mkulu wa ansembe ndi abale ake, ansembe, anayamba kumanga Chipata cha Nkhosa.+ Iwo anapatula mbali imeneyi+ ndi kuika zitseko zake. Anapatula mbali imeneyi mpaka ku Nsanja ya Meya+ ndi Nsanja ya Hananeli.+
13 Hanuni ndi anthu okhala ku Zanowa+ anakonza Chipata cha Kuchigwa.+ Iwo anachimanga ndi kuika zitseko zake,+ akapichi ake+ ndi mipiringidzo yake.+ Iwo anakonzanso mpandawo mikono* 1,000 mpaka kukafika ku Chipata cha Milu ya Phulusa.+