5 Ndiyeno pa tsiku lachitatu,+ Esitere anavala zovala zachifumu.+ Kenako anakaima m’bwalo lamkati+ la nyumba ya mfumu moyang’anana ndi nyumba ya mfumuyo. Pa nthawiyi mfumu inali itakhala pampando wake wachifumu m’nyumba yakeyo moyang’anana ndi khomo lolowera m’nyumbayo.