-
Esitere 1:6Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
6 Anapachika makatani a nsalu, makatani opangidwa ndi thonje labwino kwambiri ndi makatani abuluu.+ Makataniwo anawamanga ndi zingwe zopangidwa ndi nsalu zabwino kwambiri ndi zingwe zaubweya wa nkhosa wonyika mu utoto wofiirira.+ Zingwezi anazikulunga pamikombero yasiliva ndi pazipilala za miyala ya mabo. Anazikulunganso pamipando+ yagolide ndi siliva yokhala ngati mabedi. Mipandoyi inali pakhonde la miyala ya pofeli,* miyala yoyera ya mabo, ngale ndi miyala yakuda ya mabo.
-