45 Poyankha Davide anauza Mfilisitiyo kuti: “Iwe ukubwera kwa ine ndi lupanga, mkondo ndi nthungo,+ koma ine ndikubwera kwa iwe m’dzina la Yehova wa makamu,+ Mulungu wa asilikali a Isiraeli, amene iweyo wam’tonza.+
7 Koma ndidzachitira chifundo nyumba ya Yuda,+ ndipo Ine Yehova Mulungu wawo, ndidzawapulumutsa.+ Sindidzawapulumutsa ndi uta, lupanga, nkhondo, mahatchi* kapena ndi amuna okwera pamahatchi ayi.”+