13 Minga zidzamera pansanja zake zokhalamo. Zomera zoyabwa ndi zitsamba zaminga zidzamera pamalo ake otetezeka,+ ndipo iye adzakhala malo okhala mimbulu+ ndi bwalo la nthiwatiwa.+
7 Malo ouma chifukwa cha kutentha adzakhala dambo la madzi, ndipo malo aludzu adzakhala malo a akasupe amadzi.+ Kumalo okhala mimbulu,+ malo ake ousako, kudzakhala udzu wobiriwira, mabango ndi gumbwa.+