14 Iwowa adzamenyana ndi Mwanawankhosa,+ koma pakuti iye ndiye Mbuye wa ambuye ndi Mfumu ya mafumu,+ Mwanawankhosayo adzawagonjetsa.+ Komanso oitanidwa aja, amene ali osankhidwa mwapadera ndi okhulupirika, nawonso adzagonjetsa naye limodzi.”+
19 Ndipo ndinaona chilombo,+ mafumu+ a dziko lapansi, ndi magulu awo ankhondo atasonkhana pamodzi kuti amenyane+ ndi wokwera pahatchi+ uja ndi gulu lake lankhondo.