31 Kenako ine ndinabwera ndi akalonga+ a Yuda pampandawo. Komanso ndinaika magulu akuluakulu awiri oimba nyimbo zoyamika+ Mulungu ndiponso magulu ena oti aziwatsatira pambuyo. Gulu limodzi la oimba linali kuyenda pampandawo kudzanja lamanja molunjika Chipata cha Milu ya Phulusa.+