-
1 Mbiri 28:1Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
28 Davide anasonkhanitsa akalonga onse+ a Isiraeli ku Yerusalemu. Akalongawo+ anali a mafuko ndi a magulu otumikira mfumu, atsogoleri a magulu a anthu 1,000,+ atsogoleri a magulu a anthu 100,+ ndiponso atsogoleri oyang’anira katundu yense+ ndi ziweto+ za mfumu ndi za ana ake.+ Panalinso nduna za panyumba ya mfumu+ ndi amuna amphamvu,+ ngakhale mwamuna aliyense wamphamvu ndi wolimba mtima.
-
-
Nehemiya 9:32Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
32 “Tsopano Mulungu wathu, Mulungu wamkulu,+ wamphamvu+ ndi wochititsa mantha,+ wosunga pangano+ ndi kusonyeza kukoma mtima kosatha,+ musachepetse+ mavuto onse amene agwera ifeyo,+ mafumu athu,+ akalonga athu,+ ansembe athu,+ aneneri athu,+ makolo athu+ ndi anthu anu onse kuchokera masiku a mafumu a Asuri mpaka lero.+
-