Salimo 44:23 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 23 Nyamukani. N’chifukwa chiyani mukugonabe, inu Yehova?+Dzukani. Musatitaye kwamuyaya.+ Yesaya 64:12 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 12 Poona zinthu zonsezi, kodi mupitiriza kumangokhala osachitapo kanthu,+ inu Yehova? Kodi muzingoonerera pamene ife tikusautsidwa koopsa?+ Maliro 2:3 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 3 Mu mkwiyo wake wathyola nyanga* iliyonse ya Isiraeli.+Adani athu atatiukira, iye sanatithandize.+Mkwiyo wake ukuyakirabe Yakobo ngati moto umene wawononga ponseponse.+
12 Poona zinthu zonsezi, kodi mupitiriza kumangokhala osachitapo kanthu,+ inu Yehova? Kodi muzingoonerera pamene ife tikusautsidwa koopsa?+
3 Mu mkwiyo wake wathyola nyanga* iliyonse ya Isiraeli.+Adani athu atatiukira, iye sanatithandize.+Mkwiyo wake ukuyakirabe Yakobo ngati moto umene wawononga ponseponse.+