Salimo 141:7 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 7 Mafupa athu amwazika pakamwa pa Manda,Mofanana ndi zidutswa zimene zimamwazika pansi pamene munthu akuwaza ndi kung’amba mtengo.+ Yeremiya 14:16 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 16 Anthu amene akuwauza maulosi awowo, mitembo yawo idzatayidwa m’misewu ya Yerusalemu chifukwa cha njala ndi lupanga. Sipadzakhala wowaika m’manda, iwowo, akazi awo, ana awo aamuna ndi ana awo aakazi+ chifukwa ndidzawatsanulira tsoka pamutu pawo.’+ Yeremiya 16:4 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 4 ‘Iwo adzafa ndi matenda oopsa+ ndipo sadzawalira maliro+ kapena kuikidwa m’manda+ koma adzakhala ngati manyowa panthaka.+ Iwo adzafa ndi lupanga ndiponso njala yaikulu.+ Mitembo yawo idzakhala chakudya cha zolengedwa zouluka zam’mlengalenga ndi zilombo zakutchire.’+
7 Mafupa athu amwazika pakamwa pa Manda,Mofanana ndi zidutswa zimene zimamwazika pansi pamene munthu akuwaza ndi kung’amba mtengo.+
16 Anthu amene akuwauza maulosi awowo, mitembo yawo idzatayidwa m’misewu ya Yerusalemu chifukwa cha njala ndi lupanga. Sipadzakhala wowaika m’manda, iwowo, akazi awo, ana awo aamuna ndi ana awo aakazi+ chifukwa ndidzawatsanulira tsoka pamutu pawo.’+
4 ‘Iwo adzafa ndi matenda oopsa+ ndipo sadzawalira maliro+ kapena kuikidwa m’manda+ koma adzakhala ngati manyowa panthaka.+ Iwo adzafa ndi lupanga ndiponso njala yaikulu.+ Mitembo yawo idzakhala chakudya cha zolengedwa zouluka zam’mlengalenga ndi zilombo zakutchire.’+