18 Ana a Isiraeli sanawaphe anthuwo. Sanawaphe chifukwa atsogoleri a khamu la ana a Isiraeli anali atalumbirira+ anthuwo pali Yehova, Mulungu wa Isiraeli.+ Choncho, khamu lonse linayamba kung’ung’udza motsutsana ndi atsogoleriwo.+
35 Atangomuona, anayamba kung’amba zovala zake+ ndi kunena kuti: “Kalanga ine mwana wanga! Wandiweramitsa ndi chisoni ndipo ine ndikukupitikitsa. Ndatsegula pakamwa panga pamaso pa Yehova, ndipo sindingathe kubweza mawu anga.”+