Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Deuteronomo 23:21
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 21 “Ukapereka lonjezo kwa Yehova+ Mulungu wako usachedwe kulikwaniritsa kuopera kuti ungachimwe,+ chifukwa Yehova Mulungu wako adzafuna ndithu kuti ukwaniritse chimene walonjezacho.+

  • Salimo 15:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  4 Iye sagwirizana ndi munthu aliyense wonyansa,+

      Koma anthu oopa Yehova amawalemekeza.+

      Akalumbira kuchita zinthu zimene kenako zakhala zoipa kwa iye, sasintha malingaliro ake.+

  • Salimo 76:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Inu nonse amene mwazungulira Mulungu, lonjezani ndi kukwaniritsa malonjezo anuwo kwa Yehova Mulungu wanu.+

      Bweretsani mphatso mwamantha.+

  • Mlaliki 5:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 Ukalonjeza kwa Mulungu usamachedwe kukwaniritsa lonjezo lako,+ chifukwa palibe amene amasangalala ndi anthu opusa.+ Uzikwaniritsa zinthu zimene walonjeza.+

  • Yona 2:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  9 Koma ine, ndidzakutamandani ndi kupereka nsembe kwa inu.+

      Zimene ndalonjeza ndidzazikwaniritsa.+ Chipulumutso chimachokera kwa Yehova.”+

  • Mateyu 5:33
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 33 “Komanso munamva kuti anthu akale anauzidwa kuti, ‘Usamalumbire+ koma osachita, m’malomwake uzikwaniritsa malonjezo ako kwa Yehova.’+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena