Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Yobu 23:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Pakuti iye amadziwa bwino njira imene ine ndimadutsa.+

      Akamaliza kundiyesa, ndidzakhala ngati golide.+

  • Salimo 26:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  2 Ndisanthuleni, inu Yehova, ndi kundiyesa.+

      Yengani impso zanga ndi mtima wanga.+

  • Salimo 66:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Pakuti inu Mulungu mwatisanthula,+

      Mwatiyenga ngati siliva.+

  • Yeremiya 9:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 Choncho, Yehova wa makamu wanena kuti: “Inetu ndikuwasungunula ndipo ndiyenera kuwasanthula.+ Nanga mwana wamkazi wa anthu anga ndingamuchitirenso zotani?+

  • Zekariya 13:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 “Ine ndidzatenga gawo lachitatulo n’kuliika pamoto+ kuti liyengeke. Ndidzawayenga ngati mmene amayengera siliva+ ndi kuwayeza ngati mmene amayezera golide.+ Gawo limeneli la anthu lidzaitana dzina langa, ndipo ine ndidzawayankha.+ Ndidzanena kuti, ‘Awa ndi anthu anga,’+ ndipo iwo adzanena kuti, ‘Yehova ndi Mulungu wathu.’”+

  • Malaki 3:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Iye adzakhala pansi ngati woyenga zitsulo ndiponso ngati woyeretsa siliva.+ Adzayeretsa ana a Levi+ ndipo adzawayeretsa ngati golide+ ndi siliva. Pamene azidzapereka nsembe zawo ngati mphatso, Yehova adzaona kuti nsembe zawozo akuzipereka+ molungama.

  • 1 Petulo 1:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 Zimenezi zikukuchitikirani kuti chikhulupiriro chanu, chimene chayesedwa+ ndipo n’chamtengo wapatali kuposa golide amene amawonongekabe ngakhale kuti anadutsa m’moto,+ chidzakuchititseni kutamandidwa ndiponso kulandira ulemerero ndi ulemu, zochita za Yesu Khristu zikadzaululika.*+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena