2 Choncho anthu anapita kukamuuza Yehosafati kuti: “Kwabwera khamu lalikulu la anthu ochokera kuchigawo cha kunyanja,* ku Edomu,+ kudzamenyana nanu. Panopa iwo ali ku Hazazoni-tamara, kapena kuti ku Eni-gedi.”+
6 Koma Hamani anaona kuti n’zosakwanira kupha Moredekai yekha pakuti anthu anamuuza za anthu a mtundu wa Moredekai. Choncho Hamani anayamba kufunafuna kufafaniza+ Ayuda onse, anthu a mtundu wa Moredekai amene anali mu ufumu wonse wa Ahasiwero.+