21 Kenako iye anakambirana+ ndi anthuwo, n’kutenga anthu oimbira+ Yehova ndi omutamanda+ ovala zovala zokongola ndi zopatulika+ n’kuwaika patsogolo pa amuna onyamula zida.+ Iwo anali kunena kuti: “Tamandani Yehova,+ pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhala mpaka kalekale.”+