10 Pamene Samueli anali kupereka nsembe yopsereza, Afilisiti anayandikira kuti amenyane ndi Isiraeli. Zitatero, Yehova anachititsa mabingu amphamvu kwambiri+ pa tsiku limenelo kuti asokoneze Afilisiti.+ Choncho Afilisitiwo anagonjetsedwa pamaso pa Isiraeli.+