10 Pamenepo Yehova anasokoneza adaniwo pamaso pa Aisiraeli.+ Ndiyeno Aisiraeli anayamba kupha adaniwo kwadzaoneni ku Gibeoni,+ ndi kuwathamangitsa kulowera kuchitunda cha Beti-horoni. Ndipo anapitiriza kuwapha mpaka kukafika ku Azeka+ ndi ku Makeda.+
15 Pamenepo Yehova anayamba kusokoneza+ ndi kuwononga Sisera ndi magaleta ake onse ankhondo, pamodzi ndi anthu ake onse. Anawasokoneza ndi kuwawononga ndi lupanga pamaso pa Baraki. Zitatero Sisera anatsika m’galeta wake n’kuyamba kuthawa wapansi.