Miyambo 4:5 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 5 Upeze nzeru,+ upezenso luso lomvetsa zinthu.+ Usaiwale ndipo usapatuke pa mawu a m’kamwa mwanga.+ Miyambo 16:16 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 16 Kupeza nzeru n’kwabwino kwambiri kuposa kupeza golide.+ Ndipo ndi bwino kusankha kumvetsa zinthu kuposa siliva.+ Chivumbulutso 3:18 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 18 Chotero, ndikukulangiza kuti ugule kwa ine golide+ woyengedwa ndi moto, kuti ukhale wolemera. Ugulenso malaya akunja oyera uvale, kuti maliseche ako asaonekere+ chifukwa ungachite manyazi. Ndiponso ugule mankhwala opaka m’maso+ ako kuti uone.
16 Kupeza nzeru n’kwabwino kwambiri kuposa kupeza golide.+ Ndipo ndi bwino kusankha kumvetsa zinthu kuposa siliva.+
18 Chotero, ndikukulangiza kuti ugule kwa ine golide+ woyengedwa ndi moto, kuti ukhale wolemera. Ugulenso malaya akunja oyera uvale, kuti maliseche ako asaonekere+ chifukwa ungachite manyazi. Ndiponso ugule mankhwala opaka m’maso+ ako kuti uone.