Miyambo 1:5 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 5 Munthu wanzeru amamvetsera ndi kuphunzira malangizo owonjezereka,+ ndipo munthu womvetsa zinthu ndi amene amapeza nzeru zoyendetsera moyo wake,+ Miyambo 15:31 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 31 Munthu amene khutu lake limamvetsera chidzudzulo+ chopatsa moyo, amakhala pakati pa anthu anzeru.+ Miyambo 17:10 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 10 Kudzudzula kumam’fika pamtima munthu womvetsa zinthu,+ kuposa kukwapula munthu wopusa zikwapu 100.+ Miyambo 25:12 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 12 Munthu wanzeru akamadzudzula munthu wa khutu lomvetsera, amakhala ngati ndolo* yagolide, ndiponso ngati chokongoletsera chagolide wapadera.+ Mateyu 13:12 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 12 Pakuti amene ali nazo, adzawonjezeredwa zambiri ndipo adzakhala ndi zochuluka.+ Koma amene alibe, adzalandidwa ngakhalenso zimene ali nazo.+
5 Munthu wanzeru amamvetsera ndi kuphunzira malangizo owonjezereka,+ ndipo munthu womvetsa zinthu ndi amene amapeza nzeru zoyendetsera moyo wake,+
31 Munthu amene khutu lake limamvetsera chidzudzulo+ chopatsa moyo, amakhala pakati pa anthu anzeru.+
10 Kudzudzula kumam’fika pamtima munthu womvetsa zinthu,+ kuposa kukwapula munthu wopusa zikwapu 100.+
12 Munthu wanzeru akamadzudzula munthu wa khutu lomvetsera, amakhala ngati ndolo* yagolide, ndiponso ngati chokongoletsera chagolide wapadera.+
12 Pakuti amene ali nazo, adzawonjezeredwa zambiri ndipo adzakhala ndi zochuluka.+ Koma amene alibe, adzalandidwa ngakhalenso zimene ali nazo.+