-
Ekisodo 35:35Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
35 Iye wawapatsa mtima wanzeru+ kuti akhale amisiri aluso pa ntchito zonse za mmisiri wolinganiza kawombedwe ka nsalu+ ndi mmisiri wopeta nsalu ndi ulusi wabuluu. Wawapatsa nzeru zimenezi kutinso achite ntchito za mmisiri wopeta nsalu ndi ubweya wa nkhosa wonyika mu utoto wofiirira, ulusi wofiira kwambiri, nsalu zabwino kwambiri, ndi ntchito za mmisiri wowomba nsalu. Watero kuti akhale amuna ogwira ntchito ina iliyonse ndi kulinganiza kapangidwe ka zinthu.
-