-
1 Mafumu 22:8Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
8 Poyankha, mfumu ya Isiraeli inauza Yehosafati kuti: “Pali munthu mmodzi amene tingathe kufunsira kwa Yehova kudzera mwa iye,+ koma ineyo ndimadana naye kwambiri,+ chifukwa salosera zabwino zokhudza ine, koma zoipa.+ Munthuyo dzina lake ndi Mikaya mwana wa Imula.” Koma Yehosafati anati: “Musalankhule choncho mfumu.”+
-
-
2 Mbiri 25:16Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
16 Mneneriyo atangonena zimenezi, mfumuyo inamufunsa kuti: “Kodi tinakuika kuti ukhale mlangizi wa mfumu?+ Siya kunena zimenezi.+ Kodi ukufuna kuti akuphe?” Choncho mneneriyo anasiya, koma anati: “Ndithu ndikudziwa kuti Mulungu watsimikiza kuti akuwonongeni+ chifukwa cha zimene mwachitazi,+ ndiponso chifukwa simunamvere malangizo anga.”+
-