19 Anamanganso mizinda yake yonse yosungirako zinthu,+ mizinda yosungirako magaleta,+ mizinda ya amuna okwera pamahatchi, ndiponso zilizonse zimene iye anakonda+ kumanga ku Yerusalemu, ku Lebanoni, ndi m’dziko lonse limene ankalamulira.
15 osawerengera golide wochokera kwa amalonda oyendayenda, ndi phindu lochokera kwa amalonda, komanso golide wochokera kwa mafumu onse+ a Aluya,+ ndi kwa abwanamkubwa a m’dzikolo.