-
Zekariya 13:9Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
9 “Ine ndidzatenga gawo lachitatulo n’kuliika pamoto+ kuti liyengeke. Ndidzawayenga ngati mmene amayengera siliva+ ndi kuwayeza ngati mmene amayezera golide.+ Gawo limeneli la anthu lidzaitana dzina langa, ndipo ine ndidzawayankha.+ Ndidzanena kuti, ‘Awa ndi anthu anga,’+ ndipo iwo adzanena kuti, ‘Yehova ndi Mulungu wathu.’”+
-
-
Malaki 1:11Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
11 “Kuchokera kotulukira dzuwa kukafika kumene limalowera, dzina langa lidzakwezeka pakati pa anthu a mitundu ina.+ Kulikonse anthu azidzapereka nsembe zautsi.+ Anthu azidzapereka zopereka kapena kuti mphatso zovomerezeka polemekeza dzina langa.+ Adzachita izi chifukwa dzina langa lidzakhala lokwezeka pakati pa anthu a mitundu ina,”+ watero Yehova wa makamu.
-