19 Amene ali kolowera dzuwa adzayamba kuopa dzina la Yehova,+ ndipo amene ali kotulukira dzuwa adzaopa ulemerero wake.+ Pakuti iye adzabwera ngati mtsinje woyambitsa mavuto woyendetsedwa ndi mzimu wa Yehova.+
16 “Aliyense wotsala mwa anthu a mitundu yonse amene akubwera kudzamenyana ndi Yerusalemu,+ azidzapita kukagwadira Mfumu,+ Yehova wa makamu,+ chaka ndi chaka,+ ndi kukachita nawo chikondwerero cha misasa.+