-
Deuteronomo 31:17Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
17 Pamenepo mkwiyo wanga udzawayakira tsiku limenelo,+ ndipo ndidzawasiya+ ndi kuwabisira nkhope yanga,+ motero adzakhala chinthu choyenera kuwonongedwa. Masoka ndi zowawa zambiri zidzawagwera,+ ndipo pa tsiku limenelo adzanena kuti, ‘Masoka amenewatu akutigwera chifukwa chakuti Mulungu wathu sali pakati pathu.’+
-
-
2 Mbiri 24:20Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
20 Tsopano mzimu wa Mulungu+ unadzaza+ Zekariya+ mwana wa wansembe Yehoyada+ ndipo anaimirira pamalo okwera, n’kuyamba kuuza anthuwo kuti: “Mulungu woona wanena kuti, ‘N’chifukwa chiyani mukuphwanya malamulo a Yehova? Kodi simukuona kuti zinthu sizikukuyenderani bwino?+ Popeza mwamusiya Yehova, iyenso akusiyani.’”+
-