Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Deuteronomo 32:20
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 20 Choncho iye anati, ‘Ndiwabisire nkhope yanga,+

      Ndione kuti ziwathera bwanji.

      Pakuti iwo ndi m’badwo wokonda zoipa,+

      Ana osakhulupirika.+

  • Yobu 34:29
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 29 Iye akachititsa bata, ndani angamudzudzule?

      Ndipo akabisa nkhope yake,+ ndani angamuone?

      Kaya abisire nkhope yake mtundu+ kapena munthu, n’chimodzimodzi.

  • Salimo 27:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  9 Musandibisire nkhope yanu.+

      Musabweze mtumiki wanu mutakwiya.+

      Inu mukhale mthandizi wanga.+

      Musanditaye ndi kundisiya, inu Mulungu wa chipulumutso changa.+

  • Salimo 104:29
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 29 Mukaphimba nkhope yanu, zimasokonezeka.+

      Mukachotsa mzimu wawo, zimafa,+

      Ndipo zimabwerera kufumbi.+

  • Ezekieli 39:23
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 23 Anthu a mitundu ina adzadziwa kuti a nyumba ya Isiraeli anatengedwa kupita ku ukapolo chifukwa cha zolakwa zawo.+ Adzadziwa kuti anali kundichitira zinthu zosakhulupirika. N’chifukwa chake ine ndinawabisira nkhope yanga+ n’kuwapereka m’manja mwa adani awo ndipo onsewo anaphedwa ndi lupanga.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena