25 Pa nthawi imeneyo Yesu ananena kuti: “Ndikutamanda inu Atate pamaso pa onse, Ambuye wakumwamba ndi dziko lapansi, chifukwa mwabisira zinthu zimenezi anthu anzeru ndi ozindikira ndipo mwaziulula kwa tiana.+
11 Koma iye anawayankha kuti: “Inu mwapatsidwa mwayi wozindikira zinsinsi zopatulika+ za ufumu wakumwamba, koma anthu amenewa sanapatsidwe mwayi umenewo.+