Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Salimo 8:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  2 M’kamwa mwa ana aang’ono ndi ana oyamwa mwakhazikitsamo zamphamvu,+

      Chifukwa cha amene akukuchitirani zoipa.+

      Mwatero kuti mugonjetse mdani wanu komanso amene akufuna kukubwezerani zoipa.+

  • Yesaya 29:14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 ine ndidzachitanso zodabwitsa ndi anthu awa.+ Ndidzazichita m’njira yodabwitsa, pogwiritsira ntchito chinthu chodabwitsa. Nzeru za anthu awo anzeru zidzatha, ndipo kumvetsetsa zinthu kwa anthu awo ozindikira kudzabisika.”+

  • Mateyu 13:15
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 15 Pakuti anthu awa aumitsa mtima wawo, ndipo amva ndi makutu awo koma osalabadira. Atseka maso awo kuti asaone ndi maso awo ndi kumva ndi makutu awo ndi kuzindikira tanthauzo lake m’mitima yawo n’kutembenuka, kuti ine ndiwachiritse.’+

  • Luka 10:21
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 21 Nthawi yomweyo Yesu anakondwera+ kwambiri mwa mzimu woyera n’kunena kuti: “Atate ndikukutamandani pamaso pa onse, inu Ambuye wakumwamba ndi dziko lapansi, chifukwa zinthu izi mwazibisa kwa anzeru+ ndi ozama m’maphunziro, koma mwaziulula kwa tiana. Inde Atate, chifukwa inu munakonda kuti zinthu zikhale chonchi.

  • 1 Akorinto 1:27
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 27 Koma Mulungu anasankha zopusa za dziko+ kuti achititse manyazi anthu anzeru, ndipo Mulungu anasankha zinthu zofooka za dziko kuti achititse manyazi+ zinthu zamphamvu.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena