Salimo 94:9 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 9 Kodi amene anakupatsani makutu, sangamve?+Kapena amene anapanga maso, sangaone?+ Yesaya 45:9 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 9 Tsoka kwa amene walimbana ndi amene anamuumba,+ ngati phale limene likulimbana ndi mapale ena amene ali pansi. Kodi dongo+ lingafunse amene akuliumba kuti: “Kodi ukupanga chiyani?” Ndipo kodi chimene unapanga chinganene kuti: “Amene uja alibe manja”? Aroma 9:20 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 20 Munthu iwe!+ Iweyo ndiwe ndani kuti uziyankhana ndi Mulungu?+ Kodi chinthu choumbidwa chinganene kwa munthu amene anachiumba kuti, “Unandipangiranji motere?”+
9 Tsoka kwa amene walimbana ndi amene anamuumba,+ ngati phale limene likulimbana ndi mapale ena amene ali pansi. Kodi dongo+ lingafunse amene akuliumba kuti: “Kodi ukupanga chiyani?” Ndipo kodi chimene unapanga chinganene kuti: “Amene uja alibe manja”?
20 Munthu iwe!+ Iweyo ndiwe ndani kuti uziyankhana ndi Mulungu?+ Kodi chinthu choumbidwa chinganene kwa munthu amene anachiumba kuti, “Unandipangiranji motere?”+