Genesis 49:10 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 10 Ndodo yachifumu sidzachoka kwa Yuda,+ ndiponso chibonga cha wolamulira sichidzachoka pakati pa mapazi ake, kufikira Silo*+ atabwera. Ndipo mitundu ya anthu idzamumvera.+ Salimo 2:6 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 6 Ndipo adzanena kuti: “Inetu ndakhazika mfumu yanga+Pa Ziyoni,+ phiri langa lopatulika.”+ Salimo 45:6 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 6 Mulungu ndiye mpando wako wachifumu mpaka kalekale, ndithu mpaka muyaya.+Ndodo yako yachifumu ndiyo ndodo yachilungamo.+ Luka 1:32 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 32 Ameneyu adzakhala wamkulu+ ndipo adzatchedwa Mwana wa Wam’mwambamwamba.+ Yehova Mulungu adzam’patsa mpando wachifumu+ wa Davide atate wake.+ Yohane 1:49 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 49 Natanayeli anamuyankha kuti: “Rabi, ndinudi Mwana wa Mulungu,+ ndinu Mfumu+ ya Isiraeli.”
10 Ndodo yachifumu sidzachoka kwa Yuda,+ ndiponso chibonga cha wolamulira sichidzachoka pakati pa mapazi ake, kufikira Silo*+ atabwera. Ndipo mitundu ya anthu idzamumvera.+
6 Mulungu ndiye mpando wako wachifumu mpaka kalekale, ndithu mpaka muyaya.+Ndodo yako yachifumu ndiyo ndodo yachilungamo.+
32 Ameneyu adzakhala wamkulu+ ndipo adzatchedwa Mwana wa Wam’mwambamwamba.+ Yehova Mulungu adzam’patsa mpando wachifumu+ wa Davide atate wake.+