Salimo 45:6 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 6 Mulungu ndiye mpando wako wachifumu mpaka kalekale, ndithu mpaka muyaya.+Ndodo yako yachifumu ndiyo ndodo yachilungamo.+ Ezekieli 17:22 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 22 “‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Inenso ndidzathyola nsonga ya pamwamba penipeni pa mtengo wa mkungudza.+ Ndidzabudula nsonga yanthete kunthambi zake+ ndipo ndidzaibzala pamwamba pa phiri lalitali.+ Ezekieli 21:27 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 27 Ine ndidzawononga, ndidzawononga, ndidzawononga ufumu.*+ Ufumu umenewu sudzaperekedwa kwa wina aliyense kufikira atabwera amene ali woyenerera mwalamulo kuutenga,+ ndipo ndidzaupereka kwa iye.’+ Danieli 7:14 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 14 Kenako anamupatsa ulamuliro,+ ulemerero,+ ndi ufumu+ kuti anthu a mitundu yosiyanasiyana, olankhula zinenero zosiyanasiyana azimutumikira.+ Ulamuliro wake udzakhalapo mpaka kalekale ndipo sudzatha. Ufumu wake sudzawonongedwa.+ Yohane 1:49 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 49 Natanayeli anamuyankha kuti: “Rabi, ndinudi Mwana wa Mulungu,+ ndinu Mfumu+ ya Isiraeli.” Chivumbulutso 19:16 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 16 Pamalaya ake akunja, ngakhale pantchafu yake, anali ndi dzina lolembedwa lakuti, Mfumu ya mafumu ndi Mbuye wa ambuye.+
6 Mulungu ndiye mpando wako wachifumu mpaka kalekale, ndithu mpaka muyaya.+Ndodo yako yachifumu ndiyo ndodo yachilungamo.+
22 “‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Inenso ndidzathyola nsonga ya pamwamba penipeni pa mtengo wa mkungudza.+ Ndidzabudula nsonga yanthete kunthambi zake+ ndipo ndidzaibzala pamwamba pa phiri lalitali.+
27 Ine ndidzawononga, ndidzawononga, ndidzawononga ufumu.*+ Ufumu umenewu sudzaperekedwa kwa wina aliyense kufikira atabwera amene ali woyenerera mwalamulo kuutenga,+ ndipo ndidzaupereka kwa iye.’+
14 Kenako anamupatsa ulamuliro,+ ulemerero,+ ndi ufumu+ kuti anthu a mitundu yosiyanasiyana, olankhula zinenero zosiyanasiyana azimutumikira.+ Ulamuliro wake udzakhalapo mpaka kalekale ndipo sudzatha. Ufumu wake sudzawonongedwa.+
16 Pamalaya ake akunja, ngakhale pantchafu yake, anali ndi dzina lolembedwa lakuti, Mfumu ya mafumu ndi Mbuye wa ambuye.+