Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Genesis 49:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Ndodo yachifumu sidzachoka kwa Yuda,+ ndiponso chibonga cha wolamulira sichidzachoka pakati pa mapazi ake, kufikira Silo*+ atabwera. Ndipo mitundu ya anthu idzamumvera.+

  • Salimo 89:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  3 Mulungu anati: “Ndachita pangano ndi wosankhidwa wanga.+

      Ndalumbira kwa Davide mtumiki wanga,+

  • Salimo 110:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 110 Yehova wauza Ambuye wanga kuti:+

      “Khala kudzanja langa lamanja+

      Kufikira nditaika adani ako monga chopondapo mapazi ako.”+

  • Yesaya 9:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 Pakuti kwa ife kwabadwa mwana.+ Ife tapatsidwa mwana wamwamuna,+ ndipo paphewa pake padzakhala ulamuliro.+ Iye adzapatsidwa dzina lakuti Mlangizi Wodabwitsa,+ Mulungu Wamphamvu,+ Atate Wosatha,+ Kalonga Wamtendere.+

  • Yesaya 11:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 M’tsiku limenelo,+ padzakhala muzu wa Jese+ womwe udzaimirire ngati chizindikiro kwa anthu.+ Ngakhale anthu a mitundu ina adzatembenukira kwa iye kuti awatsogolere,+ ndipo malo ake okhalapo adzakhala aulemerero.+

  • Ezekieli 37:25
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 25 Anthu amenewa adzakhala m’dziko limene ndinapatsa mtumiki wanga Yakobo, dziko limene makolo anu anakhalamo.+ Adzakhala m’dzikomo+ pamodzi ndi ana awo ndiponso zidzukulu zawo mpaka kalekale.+ Davide mtumiki wanga adzakhala mtsogoleri wawo mpaka kalekale.+

  • Luka 1:32
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 32 Ameneyu adzakhala wamkulu+ ndipo adzatchedwa Mwana wa Wam’mwambamwamba.+ Yehova Mulungu adzam’patsa mpando wachifumu+ wa Davide atate wake.+

  • Aroma 15:12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 Komanso Yesaya anati: “Padzakhala muzu wa Jese,+ ndipo padzatuluka wina wodzalamulira mitundu.+ Mitundu idzayembekezera iye.”+

  • Chivumbulutso 5:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 Koma mmodzi wa akulu aja anandiuza kuti: “Tonthola. Taona! Mkango wa fuko la Yuda,+ muzu+ wa Davide,+ anapambana pa nkhondo+ moti iye ndiye woyenera kumatula zidindo 7 zimene amatira mpukutuwo ndi kuutsegula.”

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena