Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Salimo 2:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  6 Ndipo adzanena kuti: “Inetu ndakhazika mfumu yanga+

      Pa Ziyoni,+ phiri langa lopatulika.”+

  • Salimo 8:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  6 Munamupatsa mphamvu kuti alamulire ntchito za manja anu.+

      Mwaika zonse pansi pa mapazi ake:+

  • Salimo 89:27
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 27 Inenso ndidzamuika kukhala mwana woyamba kubadwa,+

      Ndiponso mfumu yaikulu pa mafumu onse a padziko lapansi.+

  • Salimo 110:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  2 Yehova adzatambasula ndodo+ yako yachifumu yamphamvu kuchokera m’Ziyoni+ ndi kunena kuti:

      “Pita ukagonjetse anthu pakati pa adani ako.”+

  • Yesaya 9:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 Pakuti kwa ife kwabadwa mwana.+ Ife tapatsidwa mwana wamwamuna,+ ndipo paphewa pake padzakhala ulamuliro.+ Iye adzapatsidwa dzina lakuti Mlangizi Wodabwitsa,+ Mulungu Wamphamvu,+ Atate Wosatha,+ Kalonga Wamtendere.+

  • Mateyu 28:18
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 18 Tsopano Yesu anayandikira ndi kulankhula nawo kuti: “Ulamuliro wonse+ waperekedwa kwa ine kumwamba ndi padziko lapansi.

  • Luka 10:22
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 22 Atate wanga wapereka+ zinthu zonse kwa ine, ndipo palibe amene akum’dziwa bwino Mwana koma Atate okha. Komanso Atatewo+ palibe amene akuwadziwa bwino koma Mwana+ yekha ndiponso amene Mwanayo wakonda kuwaululira za Atatewo.”

  • 1 Akorinto 15:25
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 25 Pakuti ayenera kulamulira monga mfumu kufikira Mulungu ataika adani onse pansi pa mapazi+ ake.

  • Aefeso 1:22
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 22 Mulungu anaikanso zinthu zonse pansi pa mapazi a iyeyo,+ ndipo anamuika mutu wa zinthu zonse+ chifukwa cha mpingo,

  • Chivumbulutso 3:21
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 21 Wopambana pa nkhondo+ ndidzamulola kukhala nane pampando wanga wachifumu,+ monga mmene ine ndinakhalira+ ndi Atate wanga pampando wawo wachifumu+ nditapambana pa nkhondo.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena