Danieli 7:14 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 14 Kenako anamupatsa ulamuliro,+ ulemerero,+ ndi ufumu+ kuti anthu a mitundu yosiyanasiyana, olankhula zinenero zosiyanasiyana azimutumikira.+ Ulamuliro wake udzakhalapo mpaka kalekale ndipo sudzatha. Ufumu wake sudzawonongedwa.+ Mateyu 11:27 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 27 Atate wanga wapereka zinthu zonse kwa ine, ndipo palibe amene akum’dziwa bwino Mwana koma Atate+ okha, komanso palibe amene akuwadziwa bwino Atate koma Mwana yekha+ ndi aliyense amene Mwanayo wafuna kumuululira za Atatewo.+ Aefeso 1:21 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 21 Anamuika pamwambamwamba kuposa boma lililonse, ulamuliro uliwonse, amphamvu onse, ambuye onse,+ ndi dzina lililonse loperekedwa kwa wina aliyense,+ osati mu nthawi* ino yokha,+ komanso imene ikubwerayo.+ Afilipi 2:9 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 9 Pa chifukwa chimenechinso, Mulungu anamukweza n’kumuika pamalo apamwamba.+ Ndipo anamukomera mtima n’kumupatsa dzina loposa lina lililonse.+
14 Kenako anamupatsa ulamuliro,+ ulemerero,+ ndi ufumu+ kuti anthu a mitundu yosiyanasiyana, olankhula zinenero zosiyanasiyana azimutumikira.+ Ulamuliro wake udzakhalapo mpaka kalekale ndipo sudzatha. Ufumu wake sudzawonongedwa.+
27 Atate wanga wapereka zinthu zonse kwa ine, ndipo palibe amene akum’dziwa bwino Mwana koma Atate+ okha, komanso palibe amene akuwadziwa bwino Atate koma Mwana yekha+ ndi aliyense amene Mwanayo wafuna kumuululira za Atatewo.+
21 Anamuika pamwambamwamba kuposa boma lililonse, ulamuliro uliwonse, amphamvu onse, ambuye onse,+ ndi dzina lililonse loperekedwa kwa wina aliyense,+ osati mu nthawi* ino yokha,+ komanso imene ikubwerayo.+
9 Pa chifukwa chimenechinso, Mulungu anamukweza n’kumuika pamalo apamwamba.+ Ndipo anamukomera mtima n’kumupatsa dzina loposa lina lililonse.+