Yohane 3:35 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 35 Atate amakonda Mwana wake+ ndipo anapereka zinthu zonse m’manja mwake.+ Yohane 17:2 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 2 Inu mwamupatsa ulamuliro pa anthu onse,+ kuti onse amene inu mwamupatsa,+ awapatse moyo wosatha.+ 1 Akorinto 15:27 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 27 Pakuti Mulungu “anaika zinthu zonse pansi pa mapazi ake.”+ Koma pamene akunena kuti ‘waika zinthu zonse pansi pake,’+ n’zodziwikiratu kuti sakuphatikizapo amene anaika zinthu zonsezo pansi pa iye.+
27 Pakuti Mulungu “anaika zinthu zonse pansi pa mapazi ake.”+ Koma pamene akunena kuti ‘waika zinthu zonse pansi pake,’+ n’zodziwikiratu kuti sakuphatikizapo amene anaika zinthu zonsezo pansi pa iye.+