16 koma wina mwa inu n’kunena kuti: “Yendani bwino, mupeze zovala ndi zakudya za tsiku lililonse,” koma osamupatsa zimene thupi lake likusowazo, kodi pali phindu lanji?+
17 Koma aliyense amene ali ndi zinthu zofunika pa moyo,+ n’kuona m’bale wake zikumusowa,+ koma osamusonyeza m’bale wakeyo chifundo chachikulu,+ kodi munthu ameneyu amakonda Mulungu?+