26 Pamenepo Eliyakimu+ mwana wa Hilikiya, Sebina,+ ndi Yowa+ anauza Rabisake+ kuti: “Chonde lankhulani ndi ife atumiki anu m’chilankhulo cha Asiriya+ chifukwa timachimva. Musalankhule nafe m’chilankhulo cha Ayuda,+ kuti anthu amene ali pamakomawa asamve.”