19 Ndapalana ubwenzi ndi Abulahamu kuti aphunzitse ana ake ndi mbadwa zake kuyenda m’njira ya Yehova ndi kuchita chilungamo.+ Awaphunzitse kutero, kuti Yehova adzakwaniritse kwa Abulahamu zimene ananena zokhudza iye.”+
9 “Koma khalani tcheru ndipo musamale moyo wanu,+ kuti musaiwale zinthu zimene maso anu anaona,+ ndi kuti mitima yanu isaiwale zinthu zimenezo masiku onse a moyo wanu.+ Ana anu ndi zidzukulu zanu muziwauza za zinthu zimenezo,+