36 Kenako Abigayeli anapita kwa Nabala ndipo anapeza kuti akuchita phwando m’nyumba mwake ngati phwando la mfumu.+ Nabala anali kusangalala kwambiri mumtima mwake ndipo anali ataledzereratu.+ Abigayeli sanamuuze chilichonse, chaching’ono kapena chachikulu, kufikira m’mawa mwake.