4 “‘Koma tsopano limba mtima iwe Zerubabele. Limba mtima+ iwe Yoswa mwana wa Yehozadaki mkulu wa ansembe,’ watero Yehova.
“‘Limbani mtima anthu nonse a m’dzikoli ndipo gwirani ntchito,’+ watero Yehova.
“‘Pakuti ine ndili ndi inu,’+ watero Yehova wa makamu.