15 Mukatambasula manja anu,+ ndimakubisirani maso anga.+ Ngakhale mupereke mapemphero ambiri,+ ine sindimvetsera.+ Manja anu adzaza magazi amene mwakhetsa.+
7 Kuyambira m’masiku a makolo anu mwakhala mukupatuka pa malamulo anga ndipo simunawasunge.+ Bwererani kwa ine ndipo ine ndibwerera kwa inu,”+ watero Yehova wa makamu.