17 Kuwala kwa Isiraeli+ kudzasanduka moto+ ndipo Woyera wake adzasanduka lawi la moto.+ Iye adzayaka n’kunyeketsa udzu wake* ndi zitsamba zake zaminga+ pa tsiku limodzi.
18 Siliva kapena golide wawo sadzawapulumutsa pa tsiku la mkwiyo wa Yehova.+ Moto wa mkwiyo wake udzanyeketsa dziko lonse lapansi,+ chifukwa iye adzafafaniza anthu onse okhala padziko lapansi.”+