12 Pa tsiku limenelo anthu adzabwera kwa iwe kuchokera ku Asuri ndi kumizinda ya Iguputo. Anthu ochokera ku Iguputo mpaka ku Mtsinje+ adzabwera kwa iwe. Adzabwera kuchokera m’malo onse apakati pa nyanja imodzi ndi nyanja ina, komanso pakati pa phiri limodzi ndi phiri lina.+